Mwambo wa Nsembe ya Ukaristia yotsekulira msonkhano wa ma Episkopi

Mwambo wa nsembe ya Ukaristia yotsekulira msonkhano wa aepiskopi a mpingo wa a Katolika m’maiko a Malawi, Zambia ndi Zimbabwe tsopano wayamba pa bwalo la ku likulu la apolisi m’dziko muno ku area 30 mu mzinda wa Lilongwe.

Aepiskopiwa akhala akukumana kuyambira lero m’boma la Salima komwe akhale akukambirana zinthu zosiyanasiyana zokhudza mpingowu.


Amene akutsogolera mwambo wa nsembe yamisayi ndi Ambuye George Desmond Tambala, mtsogoleri wa bungwe la aepiskopi m’Malawi.

Nthumwi ya Apapa ku maiko a Zambia ndi Malawi Ambuye Gian Luca Perici nawonso ali nawo pa mwambowu.

Wolemba: Brenard Mwanza

Scroll to Top