CDEDI ifuna Nduna itsate malamulo

Bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) lapempha m’tsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti akhazike pansi nduna yoona za Chitetezo cha m’dziko a Ken Zikhale Ng’oma, kuti ayambe kulemekeza malamulo a dziko lino komanso kusiya kuyankhula mosalabadira, komwe kungathe kubweretsa mpungwepungwe wosafunikira pa nkhani zobwezeretsa anthu othawa kwao ku misasa.
Poyankhula pa mkumano wa atolankhani lero mu mzinda wa Lilongwe, Mkulu wa CDEDI a Sylvester Namiwa ati kuyankhula kwa a Zikhale Ng’oma komanso mkulu owona za anthuwa a Ignacio Maulana kuti dziko lino likusungira akuluakulu a kale a nkhondo 44 a dziko la Rwanda, kwabweretsa mantha kwa Amalawi ambiri komanso kuonetsa kusadalirika kwa zipata zolowera ndi kutulukira m’dziko muno.
A Namiwa anapitilira kunena kuti bungwe la CDEDI likukhulupilira kuti a Zikhale Ng’oma akuyenera kufotokozera bwino Amalawi pa nkhaniyi.
[Wolemba Charity Chilanga]

Scroll to Top